Ekisodo 14:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Nthawi yomweyo Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza panyanja, ndipo kutatsala pangʼono kucha nyanjayo inayamba kubwerera mʼmalo mwake. Pamene Aiguputo ankathawa kuti madziwo asawapeze, Yehova anakankhira Aiguputowo pakatikati pa nyanja.+ Ekisodo 15:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Mwapemerera mpweya wanu, ndipo nyanja yawamiza.+Amira mʼmadzi akuya ngati chitsulo cholemera.
27 Nthawi yomweyo Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza panyanja, ndipo kutatsala pangʼono kucha nyanjayo inayamba kubwerera mʼmalo mwake. Pamene Aiguputo ankathawa kuti madziwo asawapeze, Yehova anakankhira Aiguputowo pakatikati pa nyanja.+