-
Nehemiya 9:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Choncho ana awo analowa nʼkutenga dzikolo.+ Munagonjetsa Akanani,+ anthu amʼdzikolo ndipo munawapereka mʼmanja mwawo. Munaperekanso mafumu a Akananiwo ndi anthu amʼdzikolo kwa Aisiraeli kuti awachitire zimene akufuna. 25 Iwo analanda mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ ndi dziko la nthaka yachonde.+ Ndipo anatenga zitsime zokumba kale, nyumba zodzaza ndi zinthu zabwino, minda ya mpesa, minda ya maolivi+ ndiponso mitengo yokhala ndi zipatso zambiri. Choncho ankadya nʼkukhuta moti ananenepa ndipo ankasangalala ndi ubwino wanu waukulu.
-