-
Genesis 41:39-41Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
39 Kenako Farao anauza Yosefe kuti: “Popeza kuti Mulungu wakudziwitsa zonsezi, palibenso munthu wina wozindikira ndi wanzeru ngati iwe. 40 Iweyo ukhala woyangʼanira nyumba yanga, ndipo anthu anga onse azimvera chilichonse chimene iweyo ungawauze.+ Koma ine ndekha ndikhala wamkulu kwa iwe chifukwa ndine mfumu.” 41 Farao anauzanso Yosefe kuti: “Tsopano ndikukuika kukhala woyangʼanira dziko lonse la Iguputo.”+
-
-
Genesis 41:48Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
48 Pa zaka 7 zimenezo, Yosefe anasonkhanitsa chakudya chonse chimene anakolola mʼdziko lonse la Iguputo nʼkuchisunga mʼmizinda. Mumzinda uliwonse, ankasunga chakudya chochokera mʼminda yozungulira mzindawo.
-