-
Ekisodo 9:23-26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Ndiyeno Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza kumwamba ndi ndodo yake. Atatero, Yehova anachititsa mabingu ndipo anagwetsa matalala ndi moto* padziko lapansi. Choncho Yehova anapitiriza kugwetsa matalala mʼdziko la Iguputo. 24 Ndipo kunagwa matalala komanso moto unkangʼanima. Kunagwa matalala amphamvu kwambiri amene sanaonekepo nʼkale lonse mʼdziko lonse la Iguputo.+ 25 Matalalawo anawononga china chilichonse mʼdziko lonse la Iguputo. Anapha anthu komanso nyama ndipo anawononga zomera zonse zamʼmunda. Anagwetsanso mitengo yonse yamʼdzikolo.+ 26 Koma kudera la Goseni kokha, kumene kunali Aisiraeli, sikunagwe matalala.+
-