-
Ekisodo 14:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Iwo anafunsa Mose kuti: “Kodi watibweretsa kuno kuti tidzafere mʼchipululu muno chifukwa chakuti mu Iguputo mulibe manda?+ Nʼchifukwa chiyani watichitira zimenezi? Nʼchifukwa chiyani watitulutsa mu Iguputo? 12 Kodi zimene tinkakuuza ku Iguputo kuja si zimenezi? Kodi sitinakuuze kuti, ‘Tisiye tizitumikira Aiguputoʼ? Chifukwa ndi bwino kuti tizitumikira Aiguputo kusiyana nʼkuti tifere mʼchipululu.”+
-