17 Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba;
Anandigwira nʼkundivuula mʼmadzi akuya.+
18 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,+
Kwa anthu odana nane amene anali amphamvu kuposa ine.
19 Adaniwo anandiukira pa tsiku la tsoka,+
Koma Yehova anandithandiza.
20 Ananditenga nʼkundiika pamalo otetezeka;+
Anandipulumutsa chifukwa ankasangalala nane.+