-
Mateyu 27:41-43Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
41 Chimodzimodzinso ansembe aakulu limodzi ndi alembi komanso akulu. Nawonso anayamba kumunyoza nʼkumanena kuti:+ 42 “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikumukanika! Ngati ali Mfumu ya Isiraeli,+ tiyeni tione ngati angatsike pamtengo wozunzikirapowo* ndipo ife timukhulupirira. 43 Paja iye amakhulupirira Mulungu, ndiye panopa Mulunguyo amupulumutse ngati akumufunadi+ chifukwa iye ankanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu.’”+
-
-
Luka 23:35, 36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Anthu anangoima nʼkumaonerera zimene zinkachitikazo. Koma olamulira ankamunyogodola nʼkumanena kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, musiyeni adzipulumutse yekha, ngati alidi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwa.”+ 36 Ngakhale asilikali nawonso ankamuchitira zachipongwe, ankabwera kudzamupatsa vinyo wowawasa+
-