-
Yohane 19:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Asilikaliwo atamukhomerera Yesu pamtengo, anatenga malaya ake akunja nʼkuwagawa zigawo 4, kuti msilikali aliyense atenge chigawo chimodzi. Anatenganso malaya amkati. Koma malaya amkatiwo analibe msoko, anawombedwa kuchokera pamwamba mpaka pansi. 24 Choncho iwo anakambirana kuti: “Malayawa tisawangʼambe, koma tiyeni tichite maere kuti tidziwe amene angatenge malaya amenewa.”+ Zimenezi zinachitika kuti lemba likwaniritsidwe, limene limati: “Iwo anagawana zovala zanga, ndipo anachita maere pa zovala zanga.”+ Choncho asilikaliwo anachitadi zimenezi.
-