-
Chivumbulutso 21:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu akuti: “Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu ndipo iye azidzakhala nawo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulunguyo adzakhala nawo.+ 4 Iye adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo+ ndipo imfa sidzakhalaponso.+ Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka.+ Zakalezo zapita.”
-