-
1 Timoteyo 5:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Mkazi wamasiye wolembedwa pamndandanda wa akazi amasiye, akhale wazaka zoposa 60. Akhalenso amene anali wokhulupirika kwa mwamuna wake,* 10 wodziwika kuti anachita ntchito zabwino,+ analera bwino ana ake,+ ankachereza alendo,+ anasambitsa mapazi a oyera,+ anathandiza anthu amene anali pa mavuto+ ndiponso ankagwira modzipereka ntchito iliyonse yabwino.
-
-
Tito 2:3-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Nawonso akazi achikulire akhale ndi khalidwe loyenera anthu opembedza. Asakhale amiseche, kapena akapolo a vinyo wambiri, koma akhale aphunzitsi a zinthu zabwino, 4 nʼcholinga choti azilangiza* akazi achitsikana kuti azikonda amuna awo, azikonda ana awo, 5 azikhala oganiza bwino, oyera, ogwira ntchito zapakhomo,* abwino ndiponso ogonjera amuna awo,+ kuti mawu a Mulungu asanyozedwe.
-