-
Machitidwe 16:23-25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Atawakwapula zikoti zambiri, anawatsekera mʼndende ndi kulamula woyangʼanira ndende kuti aziwalondera nʼcholinga choti asathawe.+ 24 Popeza kuti anamulamula zimenezi, iye anakawaika mʼchipinda chamkati cha ndendeyo nʼkumanga mapazi awo mʼmatangadza.
25 Koma chapakati pa usiku, Paulo ndi Sila anayamba kupemphera ndiponso kutamanda Mulungu poimba nyimbo,+ moti akaidi ena ankawamva.
-