-
2 Samueli 16:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Kenako mfumu inafunsa kuti: “Nanga mwana* wa mbuye wako ali kuti?”+ Ziba anauza mfumu kuti: “Watsala ku Yerusalemu ndipo wanena kuti, ‘Lero nyumba ya Isiraeli indibwezera ufumu wa bambo anga.’”+ 4 Kenako mfumu inauza Ziba kuti: “Zinthu zonse zimene zinali za Mefiboseti zikhale zako.”+ Ziba anati: “Ulemu wanu mfumu. Pitirizani kundikomera mtima mbuyanga mfumu.”+
-