-
Genesis 39:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Kenako, mkazi wa mbuye wake anayamba kuyangʼana Yosefe momusirira, moti ankamuuza kuti: “Ugone nane.” 8 Koma Yosefe ankakana ndipo ankauza mkazi wa mbuye wakeyo kuti: “Mbuye wanga sadera nkhawa chilichonse mʼnyumba muno chifukwa cha ine, ndipo chilichonse chimene iye ali nacho wachisiya mʼmanja mwanga. 9 Mʼnyumba muno mulibe woyangʼanira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse mʼmanja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi nʼkuchimwira Mulungu?”+
-