5 Yangʼana kumbali kuti maso ako+ asandiyangʼanitsitse,
Chifukwa akundichititsa mantha.
Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi
Zimene zikuthamanga potsika mapiri a ku Giliyadi.+
6 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa
Zimene zikuchokera kosambitsidwa,
Zonse zabereka mapasa,
Ndipo palibe imene ana ake afa.
7 Masaya ako munsalu yako yophimba kumutuyo
Ali ngati khangaza logamphula pakati.