9 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni sangalala kwambiri.
Fuula mokondwera iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu.
Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe.+
Mfumuyo ndi yolungama ndipo ikubweretsa chipulumutso.
Ndi yodzichepetsa+ ndipo ikubwera itakwera bulu.
Ikubwera itakwera mwana wamphongo wa bulu.+