-
Yesaya 14:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Yehova adzachitira chifundo Yakobo+ ndipo adzasankhanso Isiraeli.+ Iye adzachititsa kuti akhazikike* mʼdziko lawo,+ alendo adzagwirizana nawo ndipo adzakhala limodzi ndi nyumba ya Yakobo.+ 2 Anthu a mitundu ina adzawatenga nʼkubwerera nawo kwawo ndipo nyumba ya Isiraeli idzatenga anthuwo kuti akhale antchito awo aamuna ndi aakazi+ mʼdziko la Yehova. Iwo adzagwira anthu amene anawagwira nʼkupita nawo kudziko lina ndipo azidzalamulira anthu amene ankawagwiritsa ntchito mokakamiza.
-