10 Mofanana ndi mvula komanso sinowo zimene zimagwa kuchokera kumwamba
Ndipo sizibwerera kumeneko mpaka zitanyowetsa kwambiri nthaka nʼkuchititsa kuti mbewu zimere ndi kubereka zipatso,
Nʼkupereka mbewu kuti anthu adzale komanso chakudya kuti adye,
11 Ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga.+
Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake,+
Koma adzachitadi chilichonse chimene ine ndikufuna,+
Ndipo zimene ndinawatumizira kuti achite zidzachitikadi.