29 Mʼmwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo, muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni chifukwa cha machimo anu ndipo aliyense wa inu asamagwire ntchito ina iliyonse,+ kaya ndi nzika kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale.