5 Ine ndidzakhala ngati mame kwa Isiraeli,
Ndipo iye adzaphuka ngati maluwa okongola.
Mizu yake idzazama ngati mitengo ya ku Lebanoni.
6 Nthambi zake zidzatambalala,
Ulemerero wake udzakhala ngati wa mtengo wa maolivi.
Ndipo fungo lake lonunkhira lidzakhala ngati la mtengo wa ku Lebanoni.