-
Yoswa 4:21-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Kenako anauza Aisiraeli kuti: “Mʼtsogolomu ana anu akamadzafunsa abambo awo kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+ 22 Muzidzauza anawo kuti, ‘Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodano panthaka youma.+ 23 Izi zinachitika pamene Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano, mpaka iwo atawoloka. Zinachitika mofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anachita pa Nyanja Yofiira, pamene anaphwetsa madzi a nyanjayo, mpaka onse atawoloka.+ 24 Yehova anachita zimenezi kuti anthu onse apadziko lapansi adziwe kuti dzanja lake ndi lamphamvu,+ ndiponso kuti inu muziopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse.’”
-