-
2 Mbiri 20:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Choncho anthu anapita kukauza Yehosafati kuti: “Kwabwera chigulu cha anthu kuchokera kuchigawo chakunyanja,* ku Edomu,+ kudzamenyana nanu ndipo ali ku Hazazoni-tamara, kapena kuti ku Eni-gedi.”+ 3 Yehosafati atamva zimenezi anachita mantha ndipo anatsimikiza mumtima mwake kuti afunefune Yehova.+ Choncho analengeza kuti Ayuda onse asale kudya.
-
-
Esitere 4:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Esitere anayankha Moredikayi kuti: 16 “Pitani mukasonkhanitse Ayuda onse amene ali ku Susani* ndipo musale kudya+ mʼmalo mwa ine. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu,+ masana ndiponso usiku. Inenso ndi atsikana onditumikira tisala kudya. Ngakhale kuti ndi zosemphana ndi lamulo, ndidzapita kwa mfumu ndipo ngati nʼkufa, ndife.”
-