-
2 Mbiri 4:11-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Hiramu anapanganso ndowa, mafosholo ndi mbale zolowa.+
Choncho iye anamaliza ntchito imene ankagwirira Mfumu Solomo panyumba ya Mulungu woona.+ 12 Pa ntchitoyi anapanga zipilala ziwiri,+ mitu ya zipilala yooneka ngati mbale zolowa imene anaiika pamwamba pazipilala ziwirizo komanso maukonde awiri+ okutira mitu iwiri imene inali pazipilalazo. 13 Anapanganso makangaza 400+ oika pamaukonde awiri aja ndipo panali mizere iwiri ya makangaza* pa ukonde uliwonse. Makangazawo anali okutira mitu iwiri yooneka ngati mbale zolowa imene inali pazipilala ziwiri zija.+ 14 Anapanganso zotengera 10, mabeseni 10 oika pazotengerazo,+ 15 thanki imodzi, ngʼombe zamphongo 12 zokhala pansi pa thankiyo,+
-