Levitiko 26:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Ndidzabweretsa lupanga lobwezera chilango pa inu chifukwa chophwanya pangano.+ Mukadzathawira mʼmizinda yanu, ndidzabweretsa matenda pakati panu+ ndipo mudzaperekedwa mʼdzanja la mdani.+ Yeremiya 9:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 “Kodi sindikuyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” akutero Yehova. “Kodi sindikuyenera kubwezera mtundu wa anthu oterewa?+ Yeremiya 44:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Kenako Yehova sakanathanso kulekerera zinthu zoipa komanso zonyansa zimene munkachita ndipo dziko lanu linasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha ndi chotembereredwa, dziko lopanda munthu wokhalamo ngati mmene ziliri lero.+ Nahumu 1:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi wokonzeka kusonyeza mkwiyo wake.+ Yehova amabwezera adani ake,Ndipo adani ake amawasungira mkwiyo.
25 Ndidzabweretsa lupanga lobwezera chilango pa inu chifukwa chophwanya pangano.+ Mukadzathawira mʼmizinda yanu, ndidzabweretsa matenda pakati panu+ ndipo mudzaperekedwa mʼdzanja la mdani.+
9 “Kodi sindikuyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” akutero Yehova. “Kodi sindikuyenera kubwezera mtundu wa anthu oterewa?+
22 Kenako Yehova sakanathanso kulekerera zinthu zoipa komanso zonyansa zimene munkachita ndipo dziko lanu linasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha ndi chotembereredwa, dziko lopanda munthu wokhalamo ngati mmene ziliri lero.+
2 Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi wokonzeka kusonyeza mkwiyo wake.+ Yehova amabwezera adani ake,Ndipo adani ake amawasungira mkwiyo.