Deuteronomo 30:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa nʼkupita kudziko lina,+ ndipo adzakuchitirani chifundo+ nʼkukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+ Ezara 2:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Awa ndi anthu amʼchigawo* amene anatuluka mu ukapolo+ pa anthu omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anawatengera ku Babulo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense kumzinda wakwawo.+ Yeremiya 24:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Maso anga adzakhala pa iwo kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzachititsa kuti abwerere mʼdziko lino.+ Ndidzachititsa kuti zinthu ziziwayendera bwino ndipo sindidzawawononga. Ndidzawadzala ndipo sindidzawazula.+
3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa nʼkupita kudziko lina,+ ndipo adzakuchitirani chifundo+ nʼkukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+
2 Awa ndi anthu amʼchigawo* amene anatuluka mu ukapolo+ pa anthu omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anawatengera ku Babulo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense kumzinda wakwawo.+
6 Maso anga adzakhala pa iwo kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzachititsa kuti abwerere mʼdziko lino.+ Ndidzachititsa kuti zinthu ziziwayendera bwino ndipo sindidzawawononga. Ndidzawadzala ndipo sindidzawazula.+