-
1 Mbiri 9:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Pamagetiwo panali akuluakulu 4 oyangʼanira amene anaikidwa pa udindo wawo chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Iwo anali Alevi ndipo ankayangʼanira zipinda zodyera ndi chuma chamʼnyumba ya Mulungu woona.+ 27 Usiku ankakhala mʼmalo awo mozungulira nyumba yonse ya Mulungu woona chifukwa ankachita utumiki wawo waulonda. Iwowa ndi amene ankasunga makiyi nʼkumatsegula nyumbayo mʼmawa uliwonse.
-