12 Anamupatsanso mapulani a kamangidwe ka zonse zimene anauzidwa kudzera mwa mzimu zokhudza mabwalo+ a nyumba ya Yehova, zipinda zonse zodyera kuzungulira kachisi, mosungira chuma cha nyumba ya Mulungu woona ndi mosungira zinthu zimene anaziyeretsa kuti zikhale zopatulika.+