-
1 Mafumu 6:31-35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Pakhomo la chipinda chamkati anaikapo zitseko za mtengo wa paini, zipilala zamʼmbali ndiponso mafelemu, ngati mbali ya 5. 32 Zitseko ziwirizo zinali zamatabwa a mtengo wa paini ndipo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mitengo ya kanjedza ndi maluwa. Zitsekozo anazikuta ndi golide. Akerubi ndi mitengo ya kanjedza zomwe anazilemba mochita kugoba pazitsekozo anazikutanso ndi golide. 33 Anapanganso chimodzimodzi ndi khomo la kachisi,* pamafelemu ake a mtengo wa paini omwe anali mbali ya 4. 34 Anapanga zitseko ziwiri zamatabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza. Chitseko choyamba chinali ndi mbali ziwiri ndipo hafu inkatsegukira mbali ina, hafu ina inkatsegukira mbali ina. Chitseko chachiwiri chinalinso ndi mbali ziwiri ndipo hafu inkatsegukira mbali ina, hafu ina inkatsegukira mbali ina.+ 35 Pazitsekopo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mitengo ya kanjedza komanso maluwa ndipo anakuta zojambulazo ndi golide.
-