-
Levitiko 3:14-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ndipo pambuziyo azitengapo mafuta okuta matumbo ndi mafuta onse amene ali pamatumbo,+ nʼkuwapereka kwa Yehova ngati nsembe yowotcha pamoto. 15 Aziperekanso impso ziwiri zomwe zili pafupi ndi chiuno ndi mafuta okuta impsozo. Komanso azichotsa mafuta apachiwindi pamodzi ndi impsozo. 16 Wansembe aziwotcha zinthu zonsezi paguwa lansembe monga chakudya.* Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa.* Mafuta onse ndi a Yehova.+
-