6 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo+ nʼkupita nayo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo ndipo anaipatsa chigamulo. 7 Iwo anapha ana aamuna a Zedekiya iye akuona, kenako Zedekiyayo anamʼchititsa khungu. Atatero anamumanga ndi maunyolo akopa* nʼkupita naye ku Babulo.+
3 Iweyo adzakugwira ndithu nʼkukupereka kwa iye ndipo sudzathawa mʼmanja mwake.+ Udzaonana ndi mfumu ya Babulo maso ndi maso ndipo idzalankhula nawe. Iweyo udzapita ku Babulo.’+
11 Kenako mfumu ya Babulo inachititsa khungu Zedekiya,+ inamumanga ndi maunyolo akopa* nʼkupita naye ku Babulo ndipo inamuika mʼndende mpaka tsiku la imfa yake.