-
Ezekieli 33:30, 31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 Koma iwe mwana wa munthu, anthu a mtundu wako akukambirana za iwe mʼmbali mwa mpanda komanso mʼmakomo a nyumba.+ Aliyense akuuza mʼbale wake kuti, ‘Bwerani tidzamve mawu ochokera kwa Yehova.’ 31 Iwo adzasonkhana nʼkukhala pamaso pako ngati anthu anga. Adzamva mawu ako koma sadzawatsatira.+ Chifukwa ndi pakamwa pawo, amakuuza zongofuna kukusangalatsa,* koma mtima wawo ukungofuna kupeza phindu mwachinyengo.
-