-
Chivumbulutso 10:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Choncho ndinapita kwa mngeloyo nʼkumuuza kuti andipatse mpukutu waungʼonowo. Iye anandiuza kuti: “Tenga mpukutuwu udye.+ Ukupweteketsa mʼmimba, koma mʼkamwa mwako ukhala wokoma ngati uchi.” 10 Ndinatengadi mpukutu waungʼonowo mʼdzanja la mngeloyo nʼkuudya.+ Mʼkamwa mwanga unkakoma ngati uchi,+ koma nditaudya mʼmimba mwanga munayamba kupweteka.
-