2 Mafumu 25:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Iwo anapha ana aamuna a Zedekiya iye akuona, kenako Zedekiyayo anamʼchititsa khungu. Atatero anamumanga ndi maunyolo akopa* nʼkupita naye ku Babulo.+ Ezekieli 19:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Motowo unafalikira kuchokera kunthambi* zake ndipo unawotcha mphukira ndi zipatso zake,Ndipo mtengowo unalibenso nthambi zolimba komanso ndodo ya olamulira.+ Imeneyi ndi nyimbo yoimba polira ndipo idzakhala nyimbo yotchuka.’” Ezekieli 21:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chotsa nduwira ndipo vula chisoti chachifumu.+ Zinthu zasintha tsopano.+ Kweza munthu wonyozeka+ ndipo tsitsa munthu wolemekezeka.+
7 Iwo anapha ana aamuna a Zedekiya iye akuona, kenako Zedekiyayo anamʼchititsa khungu. Atatero anamumanga ndi maunyolo akopa* nʼkupita naye ku Babulo.+
14 Motowo unafalikira kuchokera kunthambi* zake ndipo unawotcha mphukira ndi zipatso zake,Ndipo mtengowo unalibenso nthambi zolimba komanso ndodo ya olamulira.+ Imeneyi ndi nyimbo yoimba polira ndipo idzakhala nyimbo yotchuka.’”
26 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chotsa nduwira ndipo vula chisoti chachifumu.+ Zinthu zasintha tsopano.+ Kweza munthu wonyozeka+ ndipo tsitsa munthu wolemekezeka.+