Yesaya 40:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Iye adzasamalira* gulu la nkhosa zake ngati mʼbusa.+ Ndi dzanja lake, adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa,Ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake. Nkhosa zimene zikuyamwitsa adzazitsogolera mwachikondi.+ Yohane 21:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Atamaliza kudya chakudya chamʼmawacho, Yesu anafunsa Simoni Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?” Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.” Iye anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.”+
11 Iye adzasamalira* gulu la nkhosa zake ngati mʼbusa.+ Ndi dzanja lake, adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa,Ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake. Nkhosa zimene zikuyamwitsa adzazitsogolera mwachikondi.+
15 Atamaliza kudya chakudya chamʼmawacho, Yesu anafunsa Simoni Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?” Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.” Iye anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.”+