-
Danieli 6:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Ine ndikulamula kuti mʼzigawo zonse za ufumu wanga, anthu azinjenjemera chifukwa cha mantha pamaso pa Mulungu wa Danieli.+ Chifukwa iye ndi Mulungu wamoyo ndipo adzakhalapo mpaka kalekale. Ufumu wake sudzawonongedwa komanso ulamuliro wake udzakhalapo kwamuyaya.+ 27 Iye amapulumutsa+ ndi kulanditsa anthu ake, ndipo amachita zizindikiro komanso zinthu zodabwitsa kumwamba ndi padziko lapansi,+ moti wapulumutsa Danieli kwa mikango.”
-