-
2 Mafumu 10:29-31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Komabe iye sanasiye kuchita machimo amene Aisiraeli ankachita chifukwa cha Yerobowamu mwana wa Nebati. Machimo ake anali akuti sanachotse mwana wa ngʼombe wagolide amene anali ku Beteli komanso amene anali ku Dani.+ 30 Choncho Yehova anauza Yehu kuti: “Chifukwa chakuti wachita bwino komanso wachita zoyenera kwa ine pochitira nyumba ya Ahabu+ zonse zimene zinali mumtima mwanga, ana ako aamuna adzakhala pampando wachifumu wa Isiraeli mpaka mʼbadwo wa 4.”+ 31 Koma Yehu sanayesetse kutsatira Chilamulo cha Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.+ Sanasiye kuchita machimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha Yerobowamu.+
-