-
Salimo 105:8-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Amakumbukira pangano lake mpaka kalekale,+
Lonjezo limene anapereka* ku mibadwo 1,000.+
9 Wakumbukira pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+
Komanso lumbiro limene analumbira kwa Isaki,+
10 Limene analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,
Komanso monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli,
11 Pamene anati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani+
Kuti likhale cholowa chako.”+
-
-
Machitidwe 3:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Inu ndinu ana a aneneri ndi a pangano limene Mulungu anapangana ndi makolo anu akale.+ Iye anauza Abulahamu kuti: ‘Kudzera mwa mbadwa* yako mabanja onse apadziko lapansi adzadalitsidwa.’+ 26 Mulungu atasankha Mtumiki wake, choyamba+ anamutumiza kwa inu, kuti adzakudalitseni pobweza aliyense wa inu kuti musiye ntchito zanu zoipa.”
-