24 Kenako Yehova anagwetsa sulufule ndi moto ngati mvula ku Sodomu ndi Gomora. Sulufule ndi motowo zinachokera kwa Yehova kumwamba.+ 25 Choncho anawononga mizindayi. Anawononga chigawo chonsecho, kuphatikizapo anthu onse okhala mʼmizindayi komanso zomera zapanthaka.+