-
Zekariya 2:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Atapatsidwa ulemerero, Mulungu wandituma kwa anthu a mitundu ina amene ankakulandani zinthu zanu,+ chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.+ 9 Ine ndidzawaloza mowaopseza, ndipo adzatengedwa ndi akapolo awo kuti akhale chuma cha akapolowo.’+ Mudzadziwa ndithu kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wandituma.
-