Yeremiya 14:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera zinthu zabodza mʼdzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo ndi masomphenya abodza, maulosi opanda pake ndi chinyengo chamumtima mwawo.+ Yeremiya 27:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 ‘Ine sindinawatume,’ akutero Yehova, ‘koma iwo akulosera zabodza mʼdzina langa. Mukawamvera ndidzakubalalitsani ndipo ndidzawononga inuyo limodzi ndi aneneri amene akulosera kwa inu.’”+
14 Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera zinthu zabodza mʼdzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo ndi masomphenya abodza, maulosi opanda pake ndi chinyengo chamumtima mwawo.+
15 ‘Ine sindinawatume,’ akutero Yehova, ‘koma iwo akulosera zabodza mʼdzina langa. Mukawamvera ndidzakubalalitsani ndipo ndidzawononga inuyo limodzi ndi aneneri amene akulosera kwa inu.’”+