-
Maliko 4:37-41Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
37 Kenako kunayamba chimphepo champhamvu chamkuntho, ndipo mafunde ankawomba ngalawayo moti inangotsala pangʼono kumira.+ 38 Koma Yesu anali kumbuyo kwa ngalawayo akugona, atatsamira pilo. Choncho anamudzutsa nʼkumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi sizikukukhudzani kuti tikufa?” 39 Atamva zimenezi anadzuka nʼkudzudzula mphepoyo komanso kuuza nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!”+ Atatero mphepoyo inaleka ndipo kenako panachita bata lalikulu. 40 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi? Kodi mudakali opandiratu chikhulupiriro?” 41 Koma iwo anagwidwa ndi mantha aakulu ndipo anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi ndani kwenikweni? Ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera.”+
-
-
Luka 8:23-25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Koma ulendowo uli mkati, Yesu anagona tulo. Kenako panyanjapo panayamba kuwomba mphepo yamkuntho, ndipo madzi anayamba kudzaza mʼngalawamo moti akanatha kumira.+ 24 Kenako anapita kukamudzutsa ndipo anamuuza kuti: “Mlangizi, Mlangizi, tikufa!” Atamva zimenezi anadzuka nʼkudzudzula mphepo ndi mafunde amphamvuwo, moti zinasiya, ndipo panyanjapo panakhala bata.+ 25 Ndiyeno anawafunsa kuti: “Chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma iwo anagwidwa ndi mantha ndipo anathedwa nzeru, moti anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi ndani kwenikweni? Nanga taonani, akutha kulamula mphepo ndi madzi ndipo zikumumvera.”+
-