-
Maliko 5:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Kenako iwo anafika kutsidya lina la nyanja, mʼdera la Agerasa.+ 2 Ndipo Yesu atangotsika mʼngalawa, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wonyansa akuchokera mʼmanda.* 3 Iye ankakonda kukhala mʼmandamo, ndipo kuyambira kalekale panalibe munthu aliyense amene anakwanitsa kumumanga ngakhale ndi unyolo koma iye osadula.
-
-
Luka 8:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Ndiyeno anaimika ngalawa ija mʼdera la Agerasa,+ tsidya linalo, moyangʼanizana ndi Galileya. 27 Yesu atangotsika nʼkufika kumtunda, anakumana ndi munthu wina wogwidwa ndi chiwanda wochokera mumzindawo. Kwa nthawi yaitali ndithu, munthuyo ankangokhala wosavala, komanso sankakhala mʼnyumba, koma kumanda.*+
-