-
Maliko 2:18-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Ophunzira a Yohane ndi Afarisi ankasala kudya. Choncho iwo anabwera kwa iye nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma ophunzira anu sasala kudya?”+ 19 Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati+ safunika kusala kudya ngati mkwatiyo ali nawo limodzi, si choncho kodi? Ngati mkwatiyo ali nawo limodzi sangasale kudya. 20 Koma masiku akubwera pamene mkwatiyo adzachotsedwa pakati pawo+ ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya.
-
-
Luka 5:33-35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Iwo anamuuza kuti: “Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri ndipo amapemphera mopembedzera. Ophunzira a Afarisi amachitanso chimodzimodzi, koma anuwa amangodya ndi kumwa.”+ 34 Yesu anawayankha kuti: “Inu simungauze anzake a mkwati kuti asale kudya pamene mkwatiyo ali nawo limodzi, mungatero ngati? 35 Koma masiku adzafika pamene mkwati+ adzachotsedwa pakati pawo. Zikadzatero, iwo adzasala kudya masiku amenewo.”+
-