-
Luka 7:31-35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 “Kodi anthu a mʼbadwo uwu ndiwayerekeze ndi ndani ndipo kodi akufanana ndi ndani?+ 32 Iwo ali ngati ana aangʼono amene akhala pansi mumsika nʼkumafuulirana kuti: ‘Tinakuimbirani chitoliro, koma simunavine. Tinalira mofuula, koma inu simunalire.’ 33 Mofanana ndi zimenezi, Yohane Mʼbatizi anabwera ndipo sakudya chakudya kapena kumwa vinyo,+ koma inu mukunena kuti: ‘Ali ndi chiwanda.’ 34 Mwana wa munthu wabwera ndipo iye akudya ndi kumwa, koma inu mukunena kuti: ‘Taonani! Munthu wosusuka ndi wokonda kwambiri vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa!’+ 35 Mulimonsemo, nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha zotsatira zake.”+
-