-
Machitidwe 28:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Mzimuwo unati, ‘Pita ukauze anthu awa kuti: “Kumva mudzamva ndithu, koma simudzazindikira. Kuyangʼana mudzayangʼana ndithu, koma simudzaona chilichonse.+ 27 Chifukwa anthu awa aumitsa mitima yawo ndipo amva ndi makutu awo, koma osalabadira. Atseka maso awo kuti asaone ndi maso awo komanso kuti asamve ndi makutu awo nʼkumvetsa tanthauzo lake mʼmitima yawo, kenako nʼkutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”’+
-