11 Koma inu mumanena kuti, ‘Munthu akauza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ndili nacho, chimene ndikanakuthandizani nacho ndi khobani (kutanthauza, mphatso yoti ndipereke kwa Mulungu),”’ 12 inu simulolanso kuti munthuyo achitire bambo ake kapena mayi ake chinthu chilichonse.+