-
Maliko 11:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ndiye ali chapatali ndithu, anaona mtengo wamkuyu umene unali ndi masamba. Iye anapita pomwepo kuti akaone ngati angapezemo kanthu. Koma atafika pamtengowo, sanapezemo chilichonse koma masamba okha basi, chifukwa sinali nyengo ya nkhuyu. 14 Choncho iye anauza mtengowo kuti: “Munthu sadzadyanso zipatso zako mpaka kalekale.”+ Ndipo ophunzira ake ankamvetsera.
-