-
Luka 3:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Yohane anayankha onsewo kuti: “Ine ndikukubatizani ndi madzi. Koma wina wamphamvu kuposa ine akubwera, amene ine sindili woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.+ Iyeyu adzakubatizani ndi mzimu woyera komanso moto.+ 17 Fosholo yake youluzira mankhusu* ili mʼmanja mwake, ndipo malo ake opunthirapo mbewu adzawayeretseratu kuti mbee! Tirigu adzamututira munkhokwe, koma mankhusu adzawawotcha ndi moto umene sungazimitsidwe.”
-