-
Machitidwe 5:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Choncho anabwera nawo nʼkuwaimika muholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda. Ndipo mkulu wa ansembe ananena 28 kuti: “Tinakulamulani mwamphamvu kuti musaphunzitsenso mʼdzina limeneli.+ Koma mwadzaza Yerusalemu yense ndi mfundo zimene mukuphunzitsa ndipo mwatsimikiza mtima kuti ife tikhale ndi mlandu wa magazi a munthu ameneyu.”+
-
-
1 Atesalonika 2:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Chifukwa inu abale munatsanzira mipingo ya Mulungu yogwirizana ndi Khristu Yesu imene ili ku Yudeya. Tikutero chifukwa munayamba kuvutitsidwa ndi anthu akwanu,+ ngati mmene iwowonso akuvutitsidwira ndi Ayuda. 15 Iwo anafika popha Ambuye Yesu+ komanso aneneri ndipo ife anatizunza.+ Kuwonjezera pamenepo, iwo sakusangalatsa Mulungu, koma akuchita zinthu zimene sizingapindulitse anthu onse.
-