-
Mateyu 15:15-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndiyeno Petulo anamupempha kuti: “Timasulireni fanizo lija.” 16 Yesu anawafunsa kuti: “Kodi inunso simunamvetse?+ 17 Kodi simukudziwa kuti chilichonse chimene chalowa mʼkamwa chimadutsa mʼmimba ndipo chimakatayidwa kuchimbudzi? 18 Koma chilichonse chimene chimatuluka pakamwa chimachokera mumtima ndipo zinthu zimenezo ndi zimene zimaipitsa munthu.+ 19 Mwachitsanzo, mumtima mumachokera maganizo oipa awa:+ maganizo a kupha anthu, a chigololo, a chiwerewere,* a kuba, maumboni onama komanso kunyoza Mulungu. 20 Zimenezi ndi zinthu zimene zimaipitsa munthu, koma kudya chakudya osasamba mʼmanja* sikuipitsa munthu.”
-