Mateyu 16:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kuuza ophunzira ake kuti iyeyo akuyenera kupita ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa kwambiri ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi ndipo akaphedwa, koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.+ Mateyu 17:22, 23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Yesu anawauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu+ 23 ndipo adzamupha. Koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+ Atamva zimenezi iwo anamva chisoni kwambiri.
21 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kuuza ophunzira ake kuti iyeyo akuyenera kupita ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa kwambiri ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi ndipo akaphedwa, koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.+
22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Yesu anawauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu+ 23 ndipo adzamupha. Koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+ Atamva zimenezi iwo anamva chisoni kwambiri.